Smith Library

Smith Library

Share

24/05/2024

ECHOES OF THE SUN

(DEAD SEEDS)

CHAPTER 7

Mam'mawa kunacha, mudzi onse kunaveka zoti kwapezeka munthu wakufa. Munthuyo panalibe ngakhale mmodzi omuzindikira chifukwa anapezeka otatemedwa nkhope yonse komaso ochotsedwa maso. Nkhani inaveka palipose mmudzi wa Dengo, mayi ake aSam mayiyu anali ndi mantha chifukwa usiku omwe anaphedwa munthuyo mwana wake sanafike pakhomo.

Thomo kumenyedwa koma anamenyedwa kuja zinafika pokagona ku chipatala admit. Anamenyedwa ndi anthu abwino ataona kuti wavulala kwambiri atamaliza kumumenya anakamusiya kuchipatala, ndikulipiraso kuthandizo kuti adzilandira treatment yabwino.
"Zoona iweyo kukanika kubwera kudzandiona?"
"Aaaah iwe Thomo bola uli moyo basi bwanji kodi milandu?"
"Koma udziwa kuti zikhakha izi ndichifukwa cha iweyo?"
"Dzinabwera chifukwa chokumenya anthu ajawa osati ine zonamizilana ayi".
"Ndiwe munthu oyipa tuluka mnyumba mwanga munoso p***ano". Thomo anadzuka pomwe anakhala ndi ndodo zake zoyendera chikhakha china ataphathikidwa ku nkhope akungooneka mbeee kuyera (white) ngati angelo.
"Man mesa tikucheza kodi?"
"Sukucheza ndine nditulukire, ndisadzakuoneso pakhomo panga pano".
"Man tad..." Thomo sanamulore nzakeyo kuti akambiraneso komaso sanamupatse mpata oti ayankhuleso ngakhale liwu limodzi. "Ndati nditulukire, zoona ineyo ndingafike apapa momwe ndililimu iweyo udziyankhula zinthu zopusa zakozo. Nditulukire sindikufuna ndiyankhuleso kachitatu".
Dzozi anatuluka manyazi atamugwira ngati munthu opezeleredwa kubafa.
"Ndiwe munthu opusa ndipo osayamika!" Anakuwa Thomo mwamkwiyo ophatikizana ndi ululu.

Amayi am'mudzi anasonkhana kunyumba kwa ma Sam kukawadekhetsa chifukwa ankangolira mosalekeza kulira mwana wawo.
"Odi kuno".
"Eya afike". Anayankha mayi wina kupeleka ulamuliro kuti munthuyo alowe ndipo munthuyo analowa.
"Sam ..." Anthu anayamba kung'ung'udza mnyumbamo atamuona munthu uja kuti anali Sam.
"Amayi mukulira chani?"
"Mwana wanga unalikuti?" Anafusa make mwana akumukumbatira mwana wakeyo.
"Ganyu emwe ndinapeza anatha mochedwa, anandipatsa malo kuti ndigone komweko chifukwa kunali kutada".
"Alemekezeke mwana wanga ulibwino".

Usiku omwe Sam anakumana ndi anyamata uja zinthu zinayenda motere.
"Ase usatichedwetsetu tikuyendera nthawi".
"Ndakuuzani kale kuti ndilibe ndalamatu".
"Kodi ukuona ngati tikucheza ndekuti?"
"Ingopangani zomwe mumakwanitsazo".
"Adhawa akuoneka ndodelera tisanawavulaze tawaunikeni kaye tionanepo nkhope pamudzi pano". Anayankhula munthu wina emwe ankaoneka wosakhudzika ndizomwe enawo ankapanga.
Anyamata sanachedwe kutulutsa ma tochi kumuunika nkhope.

"Dolo wake ndiwe kodi? Musiyeni boys adzipita". Anayankhula emwe ankaoneka otsogolera gulu loselo.
"Bwanji? Ndim'bale wanu?"
"Inuyo mungova zomwe ndukuuzanizi, musiyeni".
"Ifeyo sitikukuvetsetsani man pati".
"Tiyeni tikamusiyeso kwawo chifukwa tamuchedwa, ndikudziwa chomwe ndikupangatu kodi ineyo".
Anyamata anatengana kuuyamba ulendo umupelekeza Sam ngakhale mkuluyu analibe ndi mantha kuti kodi sakufuna akamupangire chipongwe kwina. Nanji anamudzeretsa njira ina yomwe eniwo ankayiona kufupika kukafika kwa Sam.

"Guys night patrol imeneyotu".
"Titani ndiye?"
"Asiyeni adolowa adzipita, ifeyo vuto tanyamula zikwanje".
"Mbola tikamusiya ndi nthawiyi imutenga, tiyeni tikamusiye kwathu akagona ndi mwana uja".
"Bro tabwera tivane kaye pambali ndi chiwopsezo ukufuna kutibweretseracho".
Anyamata awiri anatengana pambali kukapanga upo pa ganizo loti Sam akagone kwawo chifukwa ankaopa kuti mwina Sam akawaulula mawa akadzawaona nkhope kutacha koma winayo ananenetsa kuti zimenezo sizingachitike anabwelera kukamufusa Sam ndipo anawatsimikizira kuti ngati sipakhala kupangana chipongwe palibe chomwe anthu azadziwe chokhudza iwowo. Anatengana kumapita sanangofikira kugona anasonkha moto nkumacheza, anamuonetsa Sam malo ogona akatopa ndipo sanakhalitsepo pa motopo anapita kukagona poti anali otopa ndi ntchito zomwe anagwira pa tsikuli.

"Bwanji ndindani dolo uja komasotu ndiwachilendo ghetto ino".
Anyamatawo anayamba kufusana zokhudza Sam. Atangochoka kupita kukagona.
"Siwachilendo, dolo amene uja ndi nsilikali ali paja ndimpake simumudziwa amakhala bize ndi ntchito. Mwina mudzakumana naye tsiku lina ine palibe musadzalimbane naye".
"Zoona koma muna?"
"Khulupililirani ndukuuzani inezi".
"Koma ndodzichepetsaso kwambiri bwanji?"
"Eyaka ndimomwe amapangira asilikali".
Mkuluyo analinamiza gulu lose mmaso muli gwa chosecho anangoopa chifukwa ndi munthu anapatsidwa makhela imodzi kugwetsa nthawi yomwe anamuvutitsa Jessy uja. Nawo sanabwelereso ku zawozo anapita kukagona anagona mu boys quarter imodzi onse ndi Sam emwe ndipo anamupeza asanagone akupemphera. Mmammawa Sam anawasonkhanitsa anyamatawo, anapeza baibulo ndipo anawaphuzitsa mawu angapo ochokera mu bukhu lopatulika. Dzuwa litakwerako pang'no anakambirana zophika mmemo onsewo anasonkha kupatula Sam iyeyo sanamulore kusonkha anangodya nanji enawo ankamuopa kuti msilikali, masana ndipo ankapitano kwawo.

"Madala kumabweratu ndife abale".
"Eya ndipafupi apa tidzikupezani".
"Komaso mukamapita ku magobo mudzidzatitenga zijazi basi tasiya tamva zomwe mwatiuza zija".
"Man Chiko ndinu osangalatsa bwanji". Anayankhula Sam kwinaku gulu lonse likuseka.
"Eti Bane mesa ndikunena zoona?"
"Eya Chiko, man Sam sikuti tikukamba zocheza mudzibwera kumadzatitenga".
"Osaopa ndidzikuyankhulani akamapezeka".
Anyamatawo anamupelekeza Sam chifukwa osewo anasangalala naye munthuyo. Atakamusiya Chiko anawauza chilungamo anzakewo kuti Sam sanali nsilikali koma anamumenyako ndiye amamuopa.
"Nanusotu mulibe nyonga mpaka imodzi pansi?"
"Koditu inali punch osati masanje". Chiko anaynkhula modziyikira kumbuyo kuti anzakewo asamuseke kwambiri.
"Hahahaha ndinu wophwelerana tangovomerezani".
Anyamatawo anasekaseka ndipo onse anagwirizana kuti adzipita kwa Sam kumakacheza komaso anatsimikizika mitima kuti zoyipa asiya.

🤦‍♂️...sorry ndinabwereza part yomwe ndinaponya dzulo kungoti ndinabalalika ndi zinazake. Pepani ndithu ivani kupepesa kwa mlembi wanu

21/05/2024

ECHOES OF THE SUN

(DEAD SEEDS)

CHAPTER 5

"Abale ndukagona ine". Anayankhula hule wina akucheza ndi azinzake.
"Suze lero zachita kutani kukagona changu?"
"Amwali ndakumana ndi munthu ine eeeh ayi ngati ndinafika pobweza ndalama".
"Wooneka bwanji munthu wakeyo?"
"Wamfupi winawake".
"Ndamudziwa ineso ndikanafa".
Atsikana anacheza macheza awowo osimba munthu m'modzi kwinaku akusekana zikhakhali zawo mkati.

Macheza zibambo anali atavumba mkati nyimbo zikuphophoka mosalekeza, zizungu nazo zitamba kuyankhulidwa kale kuvina mkati. Thomo naye ndi nzake kumwa nkhani zikungotsika limodzi ndimabotolo amowa.
"Analanda kamwana uja mkulu wake ndamene akulowayo".
"Munthu ameneyoyo moti akakupatse mantha zoona mpaka kumusiya akutengere kotonola kale?"
"Ukuona kuti titani naye ndiye?"
"Tatiye komweko sangaphweketse ndiwachibwana".
"Tadikira nditsitse kaye botolo ilili".
"Ukuopatu ukatero".
"Mbola tiyeko tsopanono".
Thomo ndi Dzozi anatengana kulunjika komwe kunali bambo wadzina lake Luwisiko. Bill yawo analipira.

"Hey santa".
"Ndiweyo kodi, bwera timwe takulandira". Luwisi anayankhula mosekelera akuwapatsira mabotolo ngati kuwalandira pa tebulo yawo.
"Ukuona ngati tikufuna mowa ifeyo?" Anafusa Thomo ndinkhope yake yooneka moopseza koma anzake zamaonekedwe ake analibe nazo iwowo ankafuna macheza.
"Bwanji kodi mwabwelera zisokonezo?"
"Iweyo khala chete nzakoyu akudziwa chomwe wapanga, zisakukhudze".
"Luwi, kodi ndikuphonya chinachake pano?"
"Tangodekha iweyo, palibe kanthu kamene ukuphonyaso".
"Ukuyankhula moseka bwanji pamene anthu awawa akuoneka zokwiya?"
"Hahaha ndinkhope zawo chabe ndekuti zinangobadwa zokwiya kale".

Luwisi anapitiliza kwathira ma game anzakewo, iye analibe nazo ntchito kuti anzakewo amaoneka motani. Thomo ndi Dzozi mkwiyo unkangokwelerakwelera patadutsa kanthawi pang'ono Dzozi anamenyetsa botolo pansi kuti amubaye nalo Luwisi koma nzakeyo sanali osunthika ndizomwe zinkachitikazo iye chomwe ankakwanitsa kunali kusekelera basi. Pamalopo panafika magigo omwe ankayang'anira ngati achitetezo ku balako koma Luwisi ananenetsa kuti panalibe cholakwika chilichose pakati pa awiriwo iyeyo ndi Dzozi.

"Zomwe mukupangazi, mulakalaka mukanapanga kufika malo ano ngati simusiya". Anayankhula nzake wa Luwisi atayambano kunyasidwa ndizomwe zinkachitika pamalopo.
"Tangowasiya amenewo usalimbane nawo akatopa asiya".
"Anthu ake ifeyo ukutiyankhula zakozowo?"
"Mwinatu ukuyankhulira kusatidziwa, ukamava Dzozi uvuta munthu wake ndiineyo. Ndiyankhule bwino malo ano usanawave kuwawa chifukwa titha kukuthembetsani ndi nzanga giling'ande Thomo ali apoyu".
"lnuyotu tangokumana usadziwana tokhatokha".
"Koditu usamayankhule mopusa ngati zukukhudza rasta man". Thomo anamugwira malaya pakhosi nzake wa Luwisi koma Luwisi anali phee osakhudzika ngakhale dontho zomwe zinkachitikazo ankangovetsera ndi kuyang'ana kwinaku akutsitsira mowa wake .

Anyamata achitetezo anafikaso, apa Luwisi anawauza motsimikiza kuti chilichose chomwe chinkachitika pakati pawo anali macheza chabe komaso asafikeso pamalopo akuwasokoneza macheza awo ndimomwe amachezera. Kungoti anaphuzira college limodzi.

"Achimwene musalimbane ndi anthu amenewo kadzikangopani zanu, cholimbanirana amuna nokhanokha nkukhala chani usalimbana ndi ife bwanji?
"Tamangodutsani apa mukuyankhula ngati ndani, musaphwetseposo mtimatu kuti tiyambire kumenya inuyo".

Thomo anayamba kulimbana ndi mahule awiri omwe anayankhula akudutsa pa tebulo yomwe ankabwebweterapo, kumutero Thomo ndiye kumukweza B.P kwinaku ndekuti Dzozi atayaka moto kuyankhulana ndi anthu samamuyankha ngakhale liwu.

"Inuso ndopusa eti moti basi mwakuliramo, kutangwanika ndi anthu oti sakukuyankhani ngati ndalama zakutherani osangonyamuka kachetechete kumapita bwanji?"
"Moti ndevu zosezo basi mulibe manyazi, tamapitani uko mudzikalimbana ndi azikazi anu".
"Azibambo opusa inuso bwanji, ndinu ochititsa manyazi".
"Basi dzala kunokuno kumadzapanga phokoso kunoku mutachoka m'makwanumo".

Mahule nawo anayamba kumubwatira Thomo ndi Dzozi, kuwapangitsa kufatsa ngati mwana omupezelera akuba ndiwo muphika.

"Musamasukepotu palibe azimuna anu pano". Kuwatero mahulewo koma ndiye ngati Thomo wapala moto kudambwe koma kunali kusambulidwa ndi kutukwanidwa nkwamawa koma.
"Koditu musatipangitse kuti tikumenyeni". Thomo asanamalize ngakhale mawu akuti "Tikumenyeni" mbama inali itafika kale pa hule emwe ankayankhulitsayo. Zomwe zinapangitsa nzake wa Luwisi kukanika kuugwira, koma kupita komweko kukamumbudza Thomo zoveka bwino zija.
"Zoona ungamenye mzimayi iweyo?" Ankafusa kwina akulowetsa dzibakhera.

Naye Dzozi akuti adzinyamuka kukam***andiza nzakeyo anangozindikira spray wa tsabola ku nkhope kwake. Naye anamenyedwa musakhala bwino. Atamaliza kuwamenya anawatulutsa panja ndiwauza anyamata achitetezo kuti athane nawo koma Dzozi atapeza mpata othawa analikumba liwilo la mtondo wabooka kumusiya Thomo akusambitsidwa ndi mabakhale anthanzi, matheche mkati. Dzozi sanayimeso kapena kuyang'ana kumbuyo anakumba mpaka kunyumba kwake.

"ADzozi mwataniso nanga nkhopeyi?"
"Ndakumana ndi zifwamba nthawi yomwe ndikubwerayi".
"Nthawi zino mumachoka kuti.? Mwakumana nawo pati achifwambawo?"
"Naphiri ndisiye ndikagone ndamenyedwa kwambiri".
Mkazi wa aDzozi anakakamira kuti amuna ake amuuze chenicheni chomwe chinachitika koma ayi ndithu aDzozi zotsatira zake anamumenya nazo mbama mkazi wawoyo.

"Udzimva ndikati ndatopa". Dzozi anayankhula akupita ku chipinda kumusiya mkazi wake chiyimilire ngati chikwangwani atangogwira tsaya kulingalira pomwe analakwitsa.

"Kwinako Thomo aziona ekha kuti apanga bwanji". Anayankhula Dzozi akukokera gombeza kuti agone.

20/05/2024

Kwanuko post iyi mwayiona nthawi zanji?

20/05/2024

Pamene wayamba kuyenda mnjira, njira imaoneka

-Smith

20/05/2024

ECHOES OF THE SUN

(DEAD SEEDS)

CHAPTER 4

"Wonkhaso kuti uwu?"

Dzozi anafusa ataona nzakeyo akum***amangira. Thomo anakanika kuupeza mtima naye anaganiza kuti amulondore nzaye akasangalalilire limodzi.

"Komwe ukupita iweko".
"Ine ndimaona ngati mumafuna mkazi wangatu".
"Dzozi ziyiwale zimenezo tamangotiyeni".

Ulendo wawo unapitilira monga mwamadongosolo awo nkhani zawo zili nkhani yosatha, zomangosanjanasanjana kutha iyi kubwera iyi ngati zibakhera m'masewera ankhonya.
"Anakhala pano atachoka kalekale kungoti mkazi wanga ndiyemwe amandiyimira kutsogolo".
"Imeneyo nawe nde itiso?" Thomo anadabwitsika ndi nkhani yomwe inayambidwa kutengera kuti inaonetsa kuyambira pakati.
"Wa lendi uja, koditu amandiwawabe".
"Ukamakhala ndi mtima omafuna kugona ndi anthu alendi ako, udzazindikira manyumba ako aja mulibe anthu, adzayamba kukuthawa".
"Ukuyankhula poti ulibe malo iwe".
"Pomwe ndimakhala paja ndi plot yako?"

Apa anangokumana anthu ama plot awo okhaokha kusiyana kokhako kunali koti Dzozi anali okwatira komaso anali gwate, komaso okonda mahule. Thomo anali mamwerazi (munthu omangofuna kugulilidwa mowa). Kufanana kwako kunali koti onse anali okonda zinjoyi (zisangalalo), mowa.

"Tiyitanitse ungati?"
"Thomo chibwana apa ayi, tiyamba ndalama zako kumalizira zako".
"Paja unandiona nazo sichoncho?"
"Iwe, inetu mi..." Thomo anamupangitsa nzakeyo kusiya kuyankhula, atamulozera mkazi emwe anavala mochititsa kaso ndimopatsa chikoka. Chifikireni awiriwa kumaloku ameneyo anali bala girl oyamba kuoneka m'balamo.
"Taona katundu ase Dzozi".
"Ntchembereyo, ndikufuna kansinkhu wabwino kenakake kachipele. Komaso panopa ayi kugwe kaye ka mdima, takatenge kachaso tinayambe kaye kutsitsira tikudikira nthawi".
"Ine ndimati titsitsa wamame m'bale wanga?"
"Wamame ubwerabe ine ndikufuna ndiledzereko kaye ndi mutu winawo ndimakanika kuledzera bola ubwere pambuyo pa kachaso".
"Umwa wekha zimenezo".
"Pita ukatingere ifeyo ndiye basi, ukudikira kuti ndiyambe kuyitanitsa wamamewo".
Kunja mdima unagwa bala inayamba kudzadza anthu anasokolokasokoloka mmakomo, ena kuzintchito kukasonkhana malo amodzi ndizolinga zosiyana malingana ndizomwe aliyese amakonda mbali yake, mabwana ndi mabwana anali nawo kutsika njale zawo zabwinozabwino mongaso inali weekend. Nawo mabala girls nawo anali akuonekera mmodzim'modzi kusonjeza nthawi yokazisokora yakwana. Kwa amuna omwe amapitira mowa anali kumwa mowa, opitira zinazo anali akupanga zina zosangalatsa eniwo.

"Apatu bokha nsewu, tikumana". Anakuwa Dzozi akutenga ndi mkazi omwe anamusangalatsayo kuti adzipita ku room yake.
"Eya tikumana ine ndibadzimwetsa kaye undipeza p***ano".
Thomo anali akungotsitsa kuche kuche wake kanyama kake pambali opanda nkhawa.

"Mtsikana tabwera kuno tamusiye kapeyo". Anakuwa bambo wooneka mwa unamadya bwino ndevu zake zoyera ngati santa claus (father christmas) mimba yake ngati kambiya.
"Moti sukuona kuti wapanidwa kale?" Anafusa Dzozi akupita kotuluka ndi mkaziyo.
"Mchimwene zimenezo tangopanga zoti tinvane ndife amuna tokhatokha".
"Eya koma pa izizi kuvanakoyi".
"Mtsikana kodi wakupatsa zingati?"
"Sizugwirizana bwanji kodi? Vuto lako ndichani?" Dzozi anafusa mwa ukali.

Mtsikanayo ananena ndalama yomwe anavana ndi Dzozi ndipo mkulu winayo ananenetsa kuti apeleka kawiri ndalama imeneyo. Dzozi ngakhale ankakamirabe sizinamuphulire kanthu mtsikanayo anangomusiya ndikutengana ndi mkulu wandevu zake zoyerayo.

"Nthawi yomweyi wamaliza kale nawesotu ndiye ayitu". Thomo anayankhula kwinaku akumuseka nzakeyo kuti sanakhalitseko.
"Atilanda mkazi uja anthu andalama".
"Zakhalaso bwanji?"
Awiriwo anapitiliza macheza awo kwinaku mabotolo akungotsika, ma bill akungowerengedwa.

"Ndalama yako tenga sindikuyifunaso, dzipita". Mkulu wina anali akulimbana ndi hule wina kubwezerana ndalama mbali kufupi ndikomwe kunali ma room.

"Chavuta ndichani Suze ukubweza ndalama?" Anafusa mtsikana analandidwa aDzozi uja, atakumana ndi hule nzake akubweza ndalama.
"Ingodutsa dzipanga zako ndi customer wako mwatenganayo".
Mtsikanayo atava izi sanayankhuleso kanthu koonjezera anangopitiliza ulendo wake. Anayenda kwakanthawi ndithu kufikira pomwe anakafika ku room yake, analowa mkati mkulu uja anakhala pampando molunjika komwe kunali bed. Posakhalitsa mtsikana uja anayamba kuchotsa zovala zake.

"Dikira kaye". Anayankhula bambo uja momuyimitsa mtsikana uja atatsala ndi zovala zamkati zokha. "Zimenezo sizomwe ine ndabwelera".
"Ngati sizimenezi, mwabwelera chani?"
"Ndabwelera iweyo". M'bambo uja anadzuka ndinkhope yake yaukali manja atayika mu disenti yake ndikumalondora komwe kunali tsikanayo. Mtsikanayo zinamupatsa mantha anayamba kubwelera m'mbuyo ndimantha ndikunyamula mpeni.
"Taona, sindinabwere kudzakupanga chipongwe ndikufuna kukuthandiza". Mkuluyo anayankhula akukhala pa bed. "Dzina lako ndani?"
"Lucy". Mtsikana anayankha mwamantha.
"Ine ndi Luwisi, mosatayitsana nthawi zaka zako ndizingati ukupezeka kumalo oyipa ngati anowa chifukwa chani?"
Mtsikana uja anayamba ulira asanayankhe.
"Ineyo ndangopezeka kunoku sindikudziwaso kuti ndimadzapanga chani komano nditakuona iweyo ndinaona mwana wanga ndiwasinkhu ngati wakowo koma ali ku school". Bamboyo anatulutsa phone yake ndikumuonetsa mtsikanayo chithuzi cha mwana wakeyo.
"Makolo anga anamwalira ndimakhala ndi aunt anga, kupezeka malo anowa sikufuna. Ndimapanga izizi kuti ndidzipeza fees komaso chithandizo kwa aunt anga ndovutika komaso olumala".
"Nde utatenga matenga, ungave bwanji?"
"Ndimabwera weekend yokhayokha".

Lucy anayankhulana ndi bamboyo ngati bambo ndi mwana wake ndipo bamboyo anadzipeleka kuti adzimupangira chilichose chomwe iyeyo angachite ndikuchoka kubalako kuti wachokeratu sadzapitaso. Anamupatsa phone yomwe anagula kuti akapatse mwana wawo ndinso anamulonjeza kuti tsiku lotsatiralo adzawayimbire adzapita kwawo kukaona aunt akewo. Awiriwo anatukira limodzi, bamboyo anabwelera ku bala kuja chifukwa anasiyako nzake ndipo Lucy anatuluka anakwera njinga yamoto nkumapita.

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Address


Lilongwe