RedArc Media Blog
01/07/2026
Mayi Collen Zamba awuza komiti yakafukufuku kuti:
"A Chilima anapita mwa okha ku maliro a Ralph Kasambara."
Ndipo a Richard Chimwendo Banda ndi omwe amayenela kuyimira Dr. Lazarus Chakwera ku maliro a Kasambara.
AZamba ati ofesi ya President (OPC) sinatengeko gawo lililonse pa ulendo wa Dr. Chilima kupita ku Mzuzu.
01/07/2026
Anthu omwe akuchokela ku South Africa ndipo akusungidwa pa Joyce Chitsulo Stadium,avulaza modzi mwa ogwira ntchito ku bungwe la Red Cross komaso kuwononga katundu wina wabungweli.
Nkhani ikuti anthuwa anakwiya ati kaamba koti kakuchedwa ka ndalama zomwe amayenera kulandila kuchokera ku boma.
MIJ 📸
"No balance, free secondary school while public universities increasing tuition"- walira
01/07/2026
MAGANIZO ANU?
Ma University m'dziko muno okwana asanu aboma akweza ma fees omwe ana amapeleka, izi zili chomwechi ngakhale ophunzira ambiri sukuluzi amavutika kupeleka fees ndipo ndi ochepa okha omwe amapeza mwayi wangongole.
Ndipo zili motere:
1.LUANAR K650,000 - K1.3 Million
2.MZUNI K650,000 - K1.3 Million
3.CHANCO K650,000 - K1.3 Million
4.KUHES K1 Million - K2 Million
5.MUBAS K650,00 - K1.3 Million
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Address
Blantyre
Chichiri