Falume

Falume

Share

14/01/2025

Dear, Alembi.

Choyamba ndati ndikuthokodzeni chifukwa chopereka chilimbikitso, chiphunzitso, chidziwitso, chitonthodzo, chikondi komanso chimwemwe kudzera mu nkhani zanu,
Pitilidzani ntchito yanu popedza ikupindulira anthu ambiri mu miyoyo yathu ya tsiku ndi tsiku.

Chomwe ndalembera kalatayi kwa inu nachi,
Nditakhala pansi ndikulingalira za ntchito yotamandika yomwe mwakhala mukugwira kwa dzaka zonsezi opanda malipiro, ine ndaganidza zoti ndikathe kukupatsani kuchilimika kudzera mu ma awards,
Monga muja achitila oyimba ndi amaluso enawo, nane ndaganidza kuti chaka chino ndibweretse ma award 🏅 omwe ndawatchula kuti WRITERS AWARDS kwa mulembi aliyense yemwe amatenga mbali pakutsangalatsa anthu pano pa facebook.

Mu kuganidza kwa ine ndinazisanja kunena kuti mapeto a chaka chino tikhala ndima category awa 👇

1.BEST MALE WRITER
2.BEST FEMALE WRITER
3.MALE UPCOMING WRITER
4.FEMALE UPCOMING WRITER
5.BEST STORY OF THE YEAR
6.BEST COMBINATION WRITERS OF THE YEAR

Mmenemo ndi mmene ndaganidzila kuti ndiyambile chaka chino, ngati pali zoyenela kukonza m***a kundidziwitsa popedza munthu salephera kulakwitsa.

Ndapanga zimenezi pofuna kulimbikitsa luso lolemba nkhani limene siliwerengeredwa ngati mbali imodzi ya ntsangulutso, kotero ndatenga step imeneyi ndicholinga chofuna kudziwitsa mtundu onse kuti mu nkhani muja mulinso luso komanso ntsangulutso wapaderadera.
Ndikudziwa kuti zikhala zovuta popedza ndi chaka choyamba kupanga zimenezi, koma ndichithandidzo chochokera kwa inuyo alembi komanso awerengi tikhodza kuchikwanitsa chimenechi kuti mwina pa mmawa uzakhale umboni wathu.

Pomalidza ndafuna ndikupempheni kuti chilimikani, osafowoka popedza zokhumudwitsa sizilephera ayi,

Ndondomeko ya mmene zinthuzi ndiziyendetsere ndikhala ndikukudziwitsani ngati mungagwiridzane ndi mfundo yangayi.

Ndatha ine,
Witness Mussah.
(Falume)..............

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Phalombe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address

Phalombe