WE RUN TOWN INVESTMENT
JJB NDINYAMULE
By: Hudson Chamasowa
Ndatopa ndikupha nyerere ngati ophunzira a Yesu
Ndifuna kugula galimoto koma madobadoba asachuluke nzeru
Mwina ndipume kupalasa ndikumangoimba belu
Ogulitsa magalimoto alikuti ndiwakokere likhweru
JJB Dream Car Imports ndinyamule
Galimoto yakukhosi ndigulire
Malamulo ako onse ndiyalire
Ngati pamakhala mapepala ndipatse ndisainire
Zonse zoyenera kuchita ndifotokozere
Chilumika chino galimoto yogula iwe ndikwere
Chilungamo chako kusalala ngati tomato wa pa lizulu
Ndiwetu wosakhumudwitsa ngati malawi queens
Wachengetera ogula galimoto akuzomba ngati mowa wakwachikanda
Ku Blantyre anthu amasuka nawetu ngati pizza wogulira mkazi wamwini
Ku Salima ukupikisana ndi nyanja kusangalatsa anthu
Ku mzuzu umapezekako, wajaira chitumbuka chifukwa chokhala bwino ndi anthu
Ndiwe wovomerezeka ndi Be Forward pathukuta logula magalimo ukupukutali
Galimoto lero tingotola ngati mkazi okhumudwitsidwa ndi chibwenzi chake
Mitengo yako yonyenyeka ngati ndalama yopereka kwa anyamata a thayiming'i
Kumuganizira Malawi ndi kupeza kwake nyengo ino ya kusadabuzika kwa kwacha
Kuitanitsa galimoto ndi zipangizo zake mopanda utambwali
Kuthandizira mbalume ku MRA paulendo wochoka ku Dar Salaam
Kufotokoza m’mene galimoto ikuyendera mpaka kuno kumudzi
Kuisamutsa galimoto ku Japan popanda kuwaninkha ndalama zakunja
JJB Dream Car Imports ndinyamule.
JJB DREAM CAR Imports
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Contact the business
Telephone
Website
Address
Mzuzu
Opening Hours
| Monday | 00:00 - 23:59 |
| Tuesday | 00:00 - 23:59 |
| Wednesday | 00:00 - 23:59 |
| Thursday | 00:00 - 23:59 |
| Friday | 00:00 - 23:59 |
| Saturday | 00:00 - 23:59 |
| Sunday | 00:00 - 23:59 |